1“Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,ndinu a fuko la Yuda,inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
2Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulikandipo mumadalira Mulungu wa Israeli,amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
11Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.
12“Tamvera Ine, iwe Yakobo,Israeli, amene ndinakuyitana:Mulungu uja Woyambandi Wotsiriza ndine.
14“Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?Wokondedwa wa Yehova uja adzachitazomwe Iye anakonzera Babuloni;dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
20Tulukani mʼdziko la Babuloni!Thawani dziko la Kaldeya!Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalondipo muzilalikirempaka kumathero a dziko lapansi;muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”