1Mverani Ine, inu anthu a pa zilumbatcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
2Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwandipo anandibisa mʼchimake.
3Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
4Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchitondi kuwononga mphamvu zanga pachabe,koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
4
5Yehova anandiwumba inemʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wakekuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iyendi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
6Yehovayo tsono akuti,“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,kuti udzutse mafuko a Yakobondi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
6
7Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,Woyerayo wa Israeli akunena,amene mitundu ya anthu inamuda,amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.Akalonga nawonso adzagwada pansi.Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirikandi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
8Yehova akuti, “Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;ndinakusunga ndi kukusandutsakuti ukhale pangano kwa anthu,kuti dziko libwerere mwakalendi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
9Ndidzawuza a mʼndende kuti atulukendi a mu mdima kuti aonekere poyera.
9“Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira ndi msipu pa mʼmalo owuma.
10Iwo sadzamva njala kapena ludzu,kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolerandi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
18Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼaneana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsachimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
18
19“Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwandipo dziko lako ndi kusakazidwa,chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewerandipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
20Ana obadwa nthawi yako yachisoniadzanena kuti,‘Malo ano atichepera,tipatse malo ena woti tikhalemo.’
21Tsono iwe udzadzifunsa kuti,‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.Ndani anawalera ana amenewa?Ndinatsala ndekha,nanga awa, achokera kuti?’ ”
22Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi, “Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawondipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
23Mafumu adzakhala abambo wongokulerandipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.Iwo adzagwetsa nkhopezawo pansi.Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”