6Ndidzawusandutsa tsala,udzakhala wosatengulira ndi wosalimirandipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.Ndidzalamula mitambokuti isagwetse mvula pa mundapo.”
6
7Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonsendi Aisraeli,ndipo anthu a ku Yuda ndiwominda yake yomukondweretsa.Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
8Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,mpaka mutalanda malo onsekuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.
9Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti, “Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
10
11Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawanathamangira chakumwa choledzeretsa,amene amamwa mpaka usikukufikira ataledzera kotheratu.
12Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,matambolini, zitoliro ndi vinyo,ndipo sasamala ntchito za Yehova,salemekeza ntchito za manja ake.
13Motero anthu anga adzatengedwa ukapolochifukwa cha kusamvetsa zinthu;atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14Nʼchifukwa chake ku manda sikukhutandipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
21Tsoka kwa amene amadziona ngati anzerundipo amadziyesa ochenjera.
21
22Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyondipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphukoma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputundipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,momwemonso mizu yawo idzawolandipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
25Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakanthaMapiri akugwedezeka,ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala.
25Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;
26Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.Awo akubwera,akubweradi mofulumira kwambiri!
27Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,palibe amene akusinza kapena kugona;palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
28Mivi yawo ndi yakuthwa,mauta awo onse ndi okoka,ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
29Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,amabangula ngati misona ya mkango;imadzuma pamene ikugwira nyamandipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
30Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangulangati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.Ndipo wina akakayangʼana dzikoloadzangoona mdima ndi zovuta;ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.