1Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayianu ili kuti?Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole,ndinakugulitsani kwa ati?Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu;amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
10Ndani mwa inu amaopa Yehovandi kumvera mawu a mtumiki wake?Aliyense woyenda mu mdima,popanda chomuwunikira,iye akhulupirire dzina la Yehovandi kudalira Mulungu wake.
11Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha motondi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu,lowani mʼmoto wanu womwewo.Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa.Ndipo ine Yehovandiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.