11Anthu amene Yehova anawawombola adzabwereranakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa;chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo.Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe,chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
15Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma.Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanundipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa.Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga,ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi,ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
17Dzambatuka, dzambatuka!Imirira iwe Yerusalemu.Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyochimene Yehova anakupatsa.Iwe amene unagugudizachikho chochititsa chizwezwe.
18Mwa ana onse amene anabereka,panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera;mwa ana onse amene analera,panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
19Mavuto awiriwa akugwera iwe.Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga.Ndani angakumvere chisoni?Ndani angakutonthoze?
20Ana ako akomoka;ali lambalamba pa msewu,ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde.Ukali wa Yehovandi chidzudzulo chake zidzawagwera.
20
21Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika,iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.