6Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa;kotero adzadziwakuti ndi Ine amene ndikuyankhula,Indedi, ndine.”
6
7Ngokongoladi mapazi aamithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,chisangalalo ndi chipulumutso.Iwo akubwera kudzawuza anthua ku Ziyoni kuti,“Mulungu wako ndi mfumu!”
8Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo;akuyimba pamodzi mwachimwemwe.Popeza akuona chamasokubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
9Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe,inu mabwinja a Yerusalemu,pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,wapulumutsa Yerusalemu.
10Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulikapamaso pa anthu a mitundu yonse,ndipo anthu onse a dziko lapansiadzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
10
11Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko!Musakhudze kanthu kodetsedwa!Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehovatulukanimo ndipo mudziyeretse.
13Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yakeadzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka,chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu.Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.