3Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu,munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa,ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.
3
4Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,kumukantha ndi kumusautsa.
5Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
8Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha.Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake,poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?
9Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipandipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma,ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa,kapena kuyankhula za chinyengo.
9
10Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa.Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa.Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali,ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
11Atatha mazunzo a moyo wake,adzaona kuwala, ndipo adzakhutira.Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri,popeza adzasenza zolakwa zawo.
12Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu,adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu,popeza anapereka moyo wake mpaka kufa,ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe.Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri,ndipo anawapempherera anthu olakwa.