3“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa,inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!
4Kodi inu mukuseka yani?Kodi mukumunena ndanindi kupotoza pakamwa panu?Kodi inu si ana owukira,zidzukulu za anthu abodza?
5Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu,ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri.Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwandiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
6Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu.Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo,ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya.Kodi zimenezizingandichititse kuti ndikukomereni mtima?
7Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali.Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.
8Mʼnyumba mwanu mwayikamafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu.Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu.Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu,ndiye mwazilipira kuti mugone nazo.Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
9Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafutandi zonunkhira zochuluka.Munachita kutumiza akazembe anu kutali;inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!
10Inu mumatopa ndi maulendo anu,koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’Munapezako kumeneko zokhumba zanunʼchifukwa chake simunalefuke.
10
11“Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa,kotero kuti mwakhala mukundinamiza,ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe,kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine?Kodi mwaleka kundiopa chifukwa chotindakhala chete nthawi yayitali?
15Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse,amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo,akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika,koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtimakuti odzichepetsawo ndiwalimbitsendi kuwachotsa mantha osweka mtima.
17Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera;ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya,koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.
18Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa;kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,
19anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo.Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,”“Ndipo ndidzawachiritsa.”Akutero Yehova.
20Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka,yosatha kukhala bata,mafunde ake amaponya matope ndi ndere.
21“Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.