6Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala;ndipo chimene apangacho sangachifunde.Ntchito zawo ndi zoyipa,ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
7Amathamangira kukachita zoyipa;sachedwa kupha anthu osalakwa.Maganizo awo ndi maganizo oyipa;kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
9Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira;ndipo chipulumutso sichitifikira.Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha;tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
18Iye adzawabwezera chilango adani a anthu akemolingana ndi zimene anachita,adzaonetsa ukali kwa adani akendi kubwezera chilango odana naye.Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
19Choncho akadzabwera ngati madzioyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho.Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawaadzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
19
20“Mpulumutsi adzabwera ku Ziyonikudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,”akutero Yehova.
21Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.