1“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
2Taona, mdima waphimba dziko lapansindipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,koma Yehova adzakuwalira iwe,ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwakondipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
3
4“Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika.Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe;ana ako a amuna akubwera kuchokera kutalindipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
5Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri,mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe;chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwechuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
6Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako,ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai.Ndipo onse a ku Seba adzabweraatanyamula golide ndi lubaniuku akutamanda Yehova.
7Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu,nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani;zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe,ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
7
8“Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo,ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
9Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali;patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi,zikubweretsa ana ako ochokera kutali,pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo,kudzalemekeza Yehova Mulungu wako,Woyerayo wa Israeli,pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
11Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse,sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku,kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo,akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
12Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe;adzawonongeka kotheratu.
12
13“Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini,mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanonikuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika;ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
14Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani;onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu.Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova;Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
14
15“Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe,koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya,ndipo udzakhala malo a chimwemwecha anthu amibado yonse.
16Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthundi kuleredwa pa maere aufumu,motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako,Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
17Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa,ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo.Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwandi chitsulo mʼmalo mwa miyala.Olamulira ako adzakhala a mtendere.Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
19Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire,kapena mwezi kuti uwunikire usiku,pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya,ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20Dzuwa lako silidzalowanso,ndipo mwezi wako sudzazimiriranso;Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya,ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
21Ndipo anthu ako onse adzakhala olungamandipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya.Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala,ntchito ya manja anga,kuti aonetse ulemerero wanga.