1 Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala, ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
2 Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako. Adzakuyitanira dzina latsopano limene adzakupatse ndi Yehova.
3 Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova, ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
4 Sadzakutchanso “Wosiyidwa,” ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.” Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.” Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.” Chifukwa Yehova akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
5 Monga mnyamata amakwatira namwali, momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira; monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi, chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
5
6 Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda; sadzakhala chete usana kapena usiku. Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake musapumule.
7 Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.
7
8 Yehova analumbira atakweza dzanja lake. Anati, “Sindidzaperekanso tirigu wako kuti akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano pakuti unamuvutikira.
9 Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi ndi kutamanda Yehova, ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo mʼmabwalo a Nyumba yanga.”
9
10 Tulukani, dutsani pa zipata! Konzerani anthu njira. Lambulani, lambulani msewu waukulu! Chotsani miyala. Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.
10
11 Yehova walengeza ku dziko lonse lapansi kuti, Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti, “Taonani, chipulumutso chanu chikubwera; Yehova akubwera ndi mphotho yake akubwera nazo zokuyenerani.”
12 Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika, owomboledwa a Yehova; ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova” “Mzinda umene Yehova sanawusiye.”
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.