1Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,akuyenda mwa mphamvu zake? “Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamondiponso wamphamvu zopulumutsa.”
2Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,ngati za munthu wofinya mphesa?
2
3“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.Ndinawapondereza ndili wokwiyandipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;magazi awo anadothera pa zovala zanga,ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
4Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
7Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwakeYehova wachitira nyumba ya Israelizinthu zabwino zambiri.
9Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,anawanyamula ndikuwatengakuyambira kale lomwe.