3Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsamopanda manyazi.Iwo amapereka nsembe mʼmindandi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
4Amakatandala ku mandandipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.Amadya nyama ya nkhumba,ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
5Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
5
6“Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthuchifukwa cha machimo awo
7ndi a makolo awo,”akutero Yehova.“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapirindi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,Ine ndidzawalanga kwathunthu potsatazimene anachita kale.”
8Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesandipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;sindidzawononga onse.
9Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
10Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombekwa anthu anga ondifunafuna Ine.
10
11“Koma inu amene mumasiya Yehovandi kuyiwala phiri langa lopatulika,amene munamukonzera Gadi chakudyandi kuthirira Meni chakumwa,
17“Taonani, ndikulengamlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.Zinthu zakale sizidzakumbukika,zidzayiwalika kotheratu.
18Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyayachifukwa cha zimene ndikulenga,pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsandipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemundipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.Kumeneko sikudzamvekanso kulirandi mfuwu wodandaula.
19
20“Ana sadzafa ali akhandandipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.Wamngʼono mwa iwoadzafa ali ndi zaka 100.Amene adzalephere kufika zaka 100adzatengedwa kukhalawotembereredwa.
21Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,kapena kudzala ndi ena nʼkudya.Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyowautali ngati mitengo.Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchitoya manja awo nthawi yayitali.
23Sadzagwira ntchito pachabekapena kubereka ana kuti aone tsoka;chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.