1Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: KUSAKAZA-KWAMSANGA KUFUNKHA-KOFULUMIRA.
2Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
3Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’
4Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
5Yehova anayankhulanso ndi Ine;
6“Popeza anthu a dziko ili akanamadzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,ndipo akukondwerera Rezinindi mwana wa Remaliya,
7nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsamadzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonsendi mʼmagombe ake onse.
8Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,iwe Imanueli!”
14ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhalamwala wopunthwitsa,mwala umene umapunthwitsa anthu,thanthwe limene limagwetsa anthu.Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15Anthu ambiri adzapunthwapoadzagwa ndi kuthyokathyoka,adzakodwa ndi kugwidwa.”
15
16Manga umboniwundipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
17Ndidzayembekezera Yehova,amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
18Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
19Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo,
20kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.
21Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo.
22Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.