Yobu 25:1-6 NYCCL2016 - Bible AI

1Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2“Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.

3Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?

4Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?

5Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,

6nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
iv>