1Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.
2Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu.
3Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo;
4anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake.
5Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
6Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”
20Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene alandira amene Ine ndamutuma, alandiranso Ine. Aliyense amene alandira Ine, alandiranso amene anandituma.”
21Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”
22Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani.
23Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake.
24Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”
25Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”
26Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni.
27Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.
27Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.”
28Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye.
29Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka.
36Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”
37Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”
38Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”