9Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’
10Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake.
11Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa.
12Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate.
13Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana.
14Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.
28“Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine.