1Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane,
2(ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake).
3Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.
4Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya.
5Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.
6Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.
7Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye,
8(Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).
9Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
10Yesu anamuyankha kuti,
11Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti?
12Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”
13Yesu anayankha kuti,
14
15Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”
16Iye anamuwuza kuti,
17Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.”
18
19Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri.
20Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
21Yesu anati,
22
23
24
25Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”
26Ndipo Yesu anamuwuza kuti,
27Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
28Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu,
29“Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?”
30Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye.
31Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”
32Koma Iye anawawuza kuti,
33Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”
34Yesu anati,
35
36
37
38
39Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.”
40Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri.
41Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.
42Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”
43Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya.
44(Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake).
45Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
46Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo.
47Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
48Yesu anawawuza iwo kuti,
49Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”
50Yesu anayankha kuti,
51Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira.
52Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”
53Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye,
54Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.