Yoswa 12:1-24 NYCCL2016 - Bible AI

1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:

2Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.

3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.

5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.

6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.

7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.

8Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

9mfumu ya Yeriko — imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli — imodzi

10mfumu ya Yerusalemu — imodzi mfumu ya Hebroni — imodzi

11mfumu ya Yarimuti — imodzi mfumu ya Lakisi — imodzi

12mfumu ya Egiloni — imodzi mfumu ya Gezeri — imodzi

13mfumu ya Debri — imodzi mfumu ya Gederi — imodzi

14mfumu ya Horima — imodzi mfumu ya Aradi — imodzi

15mfumu ya Libina — imodzi mfumu ya Adulamu — imodzi

16mfumu ya Makeda — imodzi mfumu ya Beteli — imodzi

17mfumu ya Tapuwa — imodzi mfumu ya Heferi — imodzi

18mfumu ya Afeki — imodzi mfumu ya Lasaroni — imodzi

19mfumu ya Madoni — imodzi mfumu ya Hazori — imodzi

20mfumu ya Simuroni Meroni — imodzi mfumu ya Akisafu — imodzi

21mfumu ya Taanaki — imodzi mfumu ya Megido — imodzi

22mfumu ya Kadesi — imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli — imodzi

23mfumu ya Dori ku Nafoti Dori — imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala — imodzi

24mfumu ya Tiriza — imodzi — mafumu onse pamodzi analipo 31.

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
/div>