1Lizani lipenga mu Ziyoni.Chenjezani pa phiri langa loyera.Onse okhala mʼdziko anjenjemere,pakuti tsiku la Yehova likubwera,layandikira;
2tsiku la mdima ndi chisoni,tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepongakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
8Iwo sakankhanakankhana,aliyense amayenda molunjika.Amadutsa malo otchingidwapopanda kumwazikana.
9Amakhamukira mu mzinda,amathamanga mʼmbali mwa khoma.Amakwera nyumba ndi kulowamo;amalowera pa zenera ngati mbala.
9
10Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,thambo limanjenjemera,dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
11Yehova amabangulapatsogolo pawo,gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.Tsiku la Yehova ndi lalikulu;ndi loopsa.Ndani adzapirira pa tsikulo?
12“Ngakhale tsopano,bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonseposala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.
12
13Ngʼambani mtima wanuosati zovala zanu.Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
14Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,nʼkutisiyira madalitso,a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwakwa Yehova Mulungu wanu.
14
15Lizani lipenga mu Ziyoni,lengezani tsiku losala zakudya,itanitsani msonkhano wopatulika.
17Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,kuti anthu a mitundu ina awalamulire.Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”
19Yehova adzawayankha kuti, “Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafutandipo mudzakhuta ndithu;sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzokwa anthu a mitundu ina.
20“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawandi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.Ndipo mitembo yawo idzawola,fungo lake lidzamveka.”
22Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.Mitengo ikubala zipatso zake;mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
23Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,pakuti wakupatsanimvula yoyambirira mwachilungamo chake.Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
24Pa malo opunthira padzaza tirigu;mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.
24
25“Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
26Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,amene wakuchitirani zodabwitsa;ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
27Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,ndi kuti palibenso wina;ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
28“Ndipo patapita nthawi,ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,nkhalamba zanu zidzalota maloto,anyamata anu adzaona masomphenya.
29Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazindidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
30Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalengandi pa dziko lapansi,ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
31Dzuwa lidzadetsedwandipo mwezi udzaoneka ngati magazilisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.
32Ndipo aliyense amene adzayitanapa dzina la Ambuye adzapulumuka;pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyonindi mu Yerusalemu,monga Yehova wanenera,pakati pa otsalaamene Yehova wawayitana.