1“Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo,nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
2ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonsendipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati.Kumeneko ndidzawaweruzachifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli,pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthundikugawa dziko langa.
3Anagawana anthu anga pochita maerendipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere;anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyokuti iwo amwe.
4“Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu.
5Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano.
6Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
7“Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu.
8Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
9Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina:Konzekerani nkhondo!Dzutsani ankhondo amphamvu!Asilikali onse afike pafupi ndipo ayambe nkhondo.
14Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu,mʼchigwa cha chiweruzo!Pakuti tsiku la Yehova layandikiramʼchigwa cha chiweruzo.
15Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa,ndipo nyenyezi sizidzawalanso.
16Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyonindipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu;dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka.Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake,linga la anthu a ku Israeli.
17“Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu,ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.Yerusalemu adzakhala wopatulika;alendo sadzamuthiranso nkhondo.
17
18“Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano,ndipo zitunda zidzayenderera mkaka;mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi.Kasupe adzatumphuka mʼnyumba ya Yehovandipo adzathirira Chigwa cha Sitimu.
19Koma Igupto adzasanduka bwinja,Edomu adzasanduka chipululu,chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yudamʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.
20Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyayandi Yerusalemu ku mibadomibado.
21Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululukendidzakhululuka.”