5Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja,inu mtundu wa Akereti;mawu a Yehova akutsutsaiwe Kanaani, dziko la Afilisti.“Ndidzakuwonongandipo palibe amene adzatsale.”
5
6Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti,lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.
7Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda;adzapezako msipu.Nthawi ya madzulo adzagonamʼnyumba za Asikeloni.Yehova Mulungu wawo adzawasamalira;adzabwezeretsa mtendere wawo.
8“Ndamva kunyoza kwa Mowabundi chipongwe cha Amoni,amene ananyoza anthu angandi kuopseza kuti alanda dziko lawo.
9Choncho, pali Ine Wamoyo,”akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,“Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu,Amoni adzasanduka ngati Gomora;malo a zomeramera ndi maenje a mchere,dziko la bwinja mpaka muyaya.Anthu anga otsala adzawafunkha;opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
9
10Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo,chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.
11Yehova adzawachititsa mantha kwambiripamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo.Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira,uliwonse ku dziko la kwawo.
12“Inunso anthu a ku Kusi,mudzaphedwa ndi lupanga.”
14Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko,pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse.Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanunguadzakhala pa nsanamira zake.Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera,mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha,nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
15Umenewu ndiye mzinda wosasamalaumene kale unali wotetezedwa.Unkanena kuti mu mtima mwake,“Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.”Taonani lero wasanduka bwinja,kokhala nyama zakutchire!Onse owudutsa akuwunyozandi kupukusa mitu yawo.